Ndani amene ali kupanga phokoso (1) sadziwa kuti alikudzitayira nthawi (2)
muululeni kuti ndithane naye (3) ngati simutero nonsenu mudzalangidwa
(4)
1 2 3 4
A ! ? ? .
B , , ? ,
C ? ? . .
D ? . . !
CIGAWO CACITATU
Malangizo
M‟cigawo ici, funso lirilonse liri ndi ziganizo zinai zimene ziri ndi manambala
osaikidwa mu mndandanda wabwino. Ikani ziganizo izi mu m‟ndandanda wa
dongosolo labwino kuti zonenedwa zonse zikhale zomveka.
Werengani ziganizo zonse mosamala ndi kusankha njira yolongosoka motsatira
manambala kuti zikhale mudongosolo lomveka bwino.
Citsanzo: 1 kodi ndiwe munthu wa mtundu wanji
2 sitidzayenda nawenso kuyambira lero
3 wosafuna kudzisamalira
4 umangoticititsa manyazi pagulu la atsikana
A 4 3 1 2
B 3 2 4 1
C 1 3 4 2
D 2 4 3 1
Yankho “C” ndilo lolongosoka mu mumndandanda. Nkhani yonse iyenera kukhala
tere:
1 kodi ndiwe munthu wa mtundu wanji
3 wosafuna kudzisamalira
4 umangoticititsa manyazi pagulu la atsikana
2 sitidzayenda nawenso kuyambira lero